-
Levitiko 12:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yamachimo.
-
-
Levitiko 22:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 “Uza Aroni ndi ana ake komanso Aisiraeli onse kuti, ‘Mwamuna aliyense amene ndi wa Chiisiraeli kapena mlendo wokhala mu Isiraeli amene akupereka kwa Yehova nsembe yopsereza+ pofuna kukwaniritsa malonjezo ake kapena kuti ikhale nsembe yake yaufulu,+ 19 azipereka nyama yopanda chilema,+ ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo kapena mbuzi, kuti Mulungu asangalale naye. 20 Musamapereke nsembe nyama iliyonse yachilema,+ chifukwa Mulungu sangasangalale nanu.
-