-
Numeri 15:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 ndipo mukamakapereka kwa Yehova nsembe yowotcha pamoto, kaya ndi ya ngʼombe kapena ya nkhosa, kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe imene mukuipereka chifukwa cha lonjezo lapadera,+ kapena nsembe yaufulu, kapenanso nsembe imene mukupereka pa nthawi ya zikondwerero zanu,+ kuti ikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova,+
-
-
Deuteronomo 12:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+ 6 Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+
-