-
1 Samueli 2:15-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Komanso munthu wopereka nsembe asanapsereze mafuta,+ mtumiki wa wansembe ankabwera nʼkumuuza kuti: “Ndipatse nyama yosaphika ndikawotchere wansembe. Wansembe sakufuna nyama yophika koma yosaphika.” 16 Munthuyo akanena kuti: “Yembekeza kaye apsereze mafutawo+ kenako utenge chilichonse chimene ukufuna,” iye ankayankha kuti: “Ayi, ndipatse pompano, apo ayi ndichita kulanda!” 17 Atumikiwa ankachimwira Yehova kwambiri,+ chifukwa sankalemekeza nsembe ya Yehova.
-