Numeri 18:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa mʼdziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa malo pakati pawo kuti akhale cholowa chako.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisiraeli.+ Numeri 35:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Lamula Aisiraeli kuti pacholowa chawo cha malo, akapereke kwa Alevi mizinda yokhalamo.+ Akaperekenso kwa Aleviwo malo odyetserako ziweto ozungulira mizindayo.+ Numeri 35:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Malo odyetserako ziweto a mizinda imene mukapereke kwa Aleviwo, akakhale mamita 445* kuchokera pampanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonse. Deuteronomo 18:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 “Alevi omwe ndi ansembe, komanso fuko lonse la Levi, sadzapatsidwa gawo kapena cholowa pakati pa Aisiraeli. Iwo azidzadya nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, zomwe ndi cholowa chake.+
20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa mʼdziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa malo pakati pawo kuti akhale cholowa chako.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisiraeli.+
2 “Lamula Aisiraeli kuti pacholowa chawo cha malo, akapereke kwa Alevi mizinda yokhalamo.+ Akaperekenso kwa Aleviwo malo odyetserako ziweto ozungulira mizindayo.+
4 Malo odyetserako ziweto a mizinda imene mukapereke kwa Aleviwo, akakhale mamita 445* kuchokera pampanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonse.
18 “Alevi omwe ndi ansembe, komanso fuko lonse la Levi, sadzapatsidwa gawo kapena cholowa pakati pa Aisiraeli. Iwo azidzadya nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, zomwe ndi cholowa chake.+