Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 41:51, 52
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 Mwana woyambayo, Yosefe anamupatsa dzina lakuti Manase*+ chifukwa anati, “Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse ndi nyumba yonse ya bambo anga.” 52 Wachiwiriyo anamupatsa dzina lakuti Efuraimu*+ chifukwa anati, “Mulungu wandipatsa ana mʼdziko la masautso anga.”+

  • Genesis 46:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Yosefe anabereka Manase+ ndi Efuraimu+ ku Iguputo. Anabereka anawa ndi mkazi wake Asenati+ mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni.*

  • Genesis 48:17-19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Yosefe ataona kuti bambo ake aika dzanja lawo lamanja pamutu pa Efuraimu, sizinamusangalatse. Choncho, anagwira dzanja la bambo ake kuti alichotse pamutu pa Efuraimu nʼkuliika pamutu pa Manase. 18 Yosefe anauza bambo ake kuti: “Ayi bambo, musatero ayi. Mwana woyamba+ ndi uyu. Ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” 19 Koma bambo akewo anapitiriza kukana nʼkunena kuti: “Ndikudziwa mwana wanga, ndikudziwa zimenezo. Uyunso adzakhala mtundu wa anthu, ndipo adzakhala wamkulu. Koma mngʼono wakeyu adzakhala wamkulu kuposa iyeyu,+ ndipo mbadwa zake zidzachuluka kwambiri nʼkupanga mitundu ya anthu.”+

  • Numeri 2:18, 19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Amene azimanga msasa wawo kumadzulo ndi gulu la mafuko atatu la Efuraimu ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Efuraimu ndi Elisama,+ mwana wa Amihudi. 19 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 40,500.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena