51 Izi zili choncho chifukwa awirinu simunakhale okhulupirika kwa ine pakati pa Aisiraeli kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini, chifukwa simunandilemekeze pamaso pa Aisiraeli.+ 52 Iwe udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa mʼdziko limene ndikupereka kwa Aisiraeli.”+