-
Deuteronomo 12:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+ 6 Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+
-
-
Deuteronomo 16:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndipo muzidzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, Mlevi amene akukhala mumzinda wanu,* mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali pakati panu. Muzidzasangalala pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake.+
-