21 Tsopano Aisiraeli anatuma anthu kuti apite kwa Sihoni mfumu ya Aamori kukanena kuti:+ 22 “Tiloleni tidutse mʼdziko lanu. Sitikhotera mʼmunda uliwonse kapena mʼmunda wa mpesa. Sitimwa madzi pachitsime chilichonse. Tizingoyenda mu Msewu wa Mfumu mpaka titadutsa mʼdziko lanu.”+