21 Yehova anakumbukira Sara monga mmene ananenera, ndipo Yehova anachitira Sara mogwirizana ndi zimene analonjeza.+ 2 Choncho Sara anakhala woyembekezera+ ndipo anaberekera Abulahamu mwana, Abulahamuyo atakalamba. Izi zinachitika ndendende pa nthawi imene Mulungu analonjeza Abulahamu.+