Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 22:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+

      Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+

      Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+

  • 2 Mbiri 32:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu. Musachite mantha kapena kuopa mfumu ya Asuri+ ndi gulu lalikulu limene ali nalo, chifukwa ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi mfumuyo.+

  • Salimo 18:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Yehova ndi thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso amene amandipulumutsa.+

      Mulungu wanga ndi thanthwe langa+ limene ndimathawirako,

      Iye ndi chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso* komanso malo anga othawirako otetezeka.*+

  • Salimo 27:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,

      Mtima wanga sudzachita mantha.+

      Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,

      Pameneponso ndidzadalira Mulungu.

  • Salimo 46:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+

      Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.* (Selah)

  • Salimo 55:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Iye adzandipulumutsa* kwa anthu amene akundiukira nʼkundipatsa mtendere,

      Chifukwa gulu la anthu landiukira.+

  • Salimo 118:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.

      Koma mʼdzina la Yehova

      Ndinaithamangitsira kutali.

  • Aroma 8:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Ndiye tinene kuti chiyani pamenepa? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena