5 Ndithudi, mwachepetsa masiku a moyo wanga,+
Ndipo masiku a moyo wanga si kanthu pamaso panu.+
Ndithudi, munthu aliyense ngakhale ataoneka kuti ndi wotetezeka, amangokhala ngati mpweya.+ (Selah)
6 Zoonadi, moyo wa munthu aliyense umangodutsa ngati chithunzithunzi.
Iye amangovutika popanda phindu.
Amaunjika chuma, osadziwa kuti amene adzasangalale nacho ndi ndani.+