1 Mbiri 29:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Ifetu ndife alendo pamaso panu, komanso okhala mʼdziko la eni ngati mmene analili makolo athu onse.+ Masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi+ ndipo ndife osakhalitsa. Salimo 102:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka,+Ndipo ndafota ngati udzu.+ Salimo 144:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Munthu amafanana ndi mpweya.+Masiku a moyo wake ali ngati mthunzi wongodutsa.+
15 Ifetu ndife alendo pamaso panu, komanso okhala mʼdziko la eni ngati mmene analili makolo athu onse.+ Masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi+ ndipo ndife osakhalitsa.