-
2 Mafumu 9:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Zitatero Yehu anakoka uta wake nʼkubaya Yehoramu kumsana pakati pamapewa mpaka muviwo unatulukira pamtima pake ndipo Yehoramu anagwa mʼgaleta lake lankhondo.
-
-
Luka 11:49-51Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
49 Nʼchifukwa chake nzeru ya Mulungu inanenanso kuti: ‘Ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, koma iwo adzapha komanso kuzunza ena mwa iwo. 50 Choncho mʼbadwo uwu udzaimbidwa mlandu wa magazi a aneneri, amene anakhetsedwa kuyambira pamene dziko linakhazikika.+ 51 Kuyambira magazi a Abele+ mpaka magazi a Zekariya, amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi nyumba yopatulika.’*+ Inde ndikukuuzani, mʼbadwo uwu udzayankha mlandu wa magazi amenewo.
-