Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 6:10-12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsani,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yabwino imene simunamange ndinu,+ 11 yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zosiyanasiyana zabwino zimene simunagwirire ntchito, zitsime zimene simunakumbe ndinu komanso minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale ndinu, ndiye mukakadya nʼkukhuta,+ 12 mukasamale kuti musakaiwale Yehova+ amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.

  • Yobu 31:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ngati ndikudalira golide,

      Kapena kuuza golide woyenga bwino kuti, ‘Ndimadalira iwe.’+

  • Yobu 31:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Chimenecho chikanakhala cholakwa chimene oweruza akuyenera kundipatsira chilango,

      Chifukwa ndikanakhala nditakana Mulungu woona wakumwamba.

  • Miyambo 11:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Chuma chidzakhala chopanda* phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+

      Koma chilungamo nʼchimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+

  • Miyambo 11:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Munthu amene amadalira chuma chake adzakumana ndi mavuto,+

      Koma anthu olungama adzasangalala ngati mtengo wa masamba obiriwira.+

  • Miyambo 23:4, 5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Usadzitopetse pofuna kupeza chuma.+

      Leka kuchita zimenezi, mʼmalomwake uzisonyeza kuti ndiwe womvetsa zinthu.*

       5 Ukayangʼana pamene panali chumacho, umapeza kuti palibe,+

      Chifukwa ndithu chimamera mapiko ngati chiwombankhanga nʼkuulukira mʼmwamba.+

  • Mateyu 6:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Siyani kudziunjikira chuma padziko lapansi,+ pomwe njenjete* komanso dzimbiri zimawononga ndiponso pomwe akuba amathyola nʼkuba.

  • Mateyu 6:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Kapolo sangatumikire ambuye awiri, chifukwa akhoza kudana ndi mmodzi nʼkukonda winayo,+ kapena angakhale wokhulupirika kwa mmodzi nʼkunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.+

  • Maliko 8:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake?+

  • Luka 12:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi dyera* lamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera mʼzinthu zimene ali nazo.”+

  • 1 Timoteyo 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ulangize* anthu achuma mʼdzikoli* kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika,+ koma azidalira Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse zomwe timasangalala nazo.+

  • 1 Yohane 2:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Chifukwa chilichonse chamʼdzikoli, monga zimene thupi limalakalaka,+ zimene maso amalakalaka+ komanso kudzionetsera ndi zinthu zimene munthu ali nazo pa moyo wake,* sizichokera kwa Atate koma mʼdzikoli.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena