-
Chivumbulutso 20:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inatambasulidwa. Koma panali mpukutu wina umene unatambasulidwa, womwe ndi mpukutu wa moyo.+ Akufa anaweruzidwa potengera zimene zinalembedwa mʼmipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.+ 13 Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Imfa komanso Manda* zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense payekha anaweruzidwa mogwirizana ndi ntchito zake.+
-