-
Yoswa 24:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndinawachititsa mantha inu musanafike, choncho anakuthawani+ ngati mmene anachitira mafumu awiri a Aamori. Iwo sanathawe chifukwa cha lupanga lanu kapena chifukwa cha uta wanu.+ 13 Ndinakupatsani dziko limene simunalikhetsere thukuta komanso mizinda imene simunaimange,+ ndipo munayamba kukhalamo. Mukudyanso zipatso za mitengo ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale.’+
-
-
1 Mafumu 4:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Ayuda ndi Aisiraeli ankakhala mwamtendere. Aliyense ankakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu, kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba, masiku onse a Solomo.
-