Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 33:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ndiwe wosangalala iwe Isiraeli!+

      Ndani angafanane ndi iwe,+

      Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+

      Chishango chako chokuteteza,+

      Komanso lupanga lako lamphamvu?

      Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+

      Ndipo iwe udzaponda pamisana yawo.”*

  • 2 Samueli 22:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Mulungu wanga ndi thanthwe langa,+ ine ndimathawira kwa iye,

      Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga ya chipulumutso* ndi malo anga achitetezo.*+

      Komanso ndi malo anga othawirako,+ mpulumutsi wanga+ amene amandipulumutsa kwa anthu achiwawa.

  • Salimo 144:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Iye amandisonyeza chikondi chake chokhulupirika ndipo ndi malo anga otetezeka,

      Malo anga othawirako otetezeka* komanso amene amandipulumutsa,

      Chishango changa ndiponso malo amene ndathawirako kuti nditetezeke,+

      Amene amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena