Ekisodo 19:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Pa tsiku lachitatu mʼmawa, kunachita mabingu ndi mphezi ndipo mtambo wakuda+ unakuta phiri. Kunamvekanso kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, moti anthu onse mumsasawo anayamba kunjenjemera.+ Ekisodo 19:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Phiri la Sinai linafuka utsi paliponse, chifukwa chakuti Yehova anabwera paphiripo mʼmoto.+ Utsi wakewo unkakwera kumwamba ngati utsi wa uvuni ndipo phiri lonse linkanjenjemera kwambiri.+ Salimo 77:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Phokoso la bingu lanu+ linali ngati la mawilo a galeta.Kungʼanima kwa mphezi kunaunika padziko lapansi.+Dziko lapansi linanjenjemera komanso kugwedezeka.+ Salimo 104:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+
16 Pa tsiku lachitatu mʼmawa, kunachita mabingu ndi mphezi ndipo mtambo wakuda+ unakuta phiri. Kunamvekanso kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, moti anthu onse mumsasawo anayamba kunjenjemera.+
18 Phiri la Sinai linafuka utsi paliponse, chifukwa chakuti Yehova anabwera paphiripo mʼmoto.+ Utsi wakewo unkakwera kumwamba ngati utsi wa uvuni ndipo phiri lonse linkanjenjemera kwambiri.+
18 Phokoso la bingu lanu+ linali ngati la mawilo a galeta.Kungʼanima kwa mphezi kunaunika padziko lapansi.+Dziko lapansi linanjenjemera komanso kugwedezeka.+