Salimo 43:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+ Zimenezi zinditsogolere.+Zinditsogolere kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+ Miyambo 6:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Chifukwa lamulolo ndi nyale,+Ndipo malangizo ndi kuwala,+Komanso kudzudzula kumene kumathandiza munthu kusintha ndi njira yakumoyo.+ Yesaya 51:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Inu anthu anga, ndimvereni.Iwe mtundu wanga,+ tchera khutu kwa ine. Chifukwa kwa ine kudzachokera lamulo+Ndipo ndidzachititsa kuti chilungamo changa chikhazikike ngati kuwala ku mitundu ya anthu.+ Aroma 15:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.+ Malembawa amatithandiza kupirira+ ndiponso amatilimbikitsa nʼcholinga choti tikhale ndi chiyembekezo.+ 2 Timoteyo 3:16, 17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi othandiza pophunzitsa,+ kudzudzula, kukonza zinthu ndi kulangiza mwachilungamo,+ 17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera kwambiri ndi wokonzeka mokwanira kugwira ntchito iliyonse yabwino. 2 Petulo 1:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Nʼchifukwa chake sitikayikira ngakhale pangʼono kuti mawu aulosiwa adzakwaniritsidwa ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewa aziwala mʼmitima yanu ngati nyale+ imene ikuwala mumdima. Pitirizani kuchita zimenezi mpaka mʼbandakucha, nthanda*+ itatuluka.
3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+ Zimenezi zinditsogolere.+Zinditsogolere kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+
23 Chifukwa lamulolo ndi nyale,+Ndipo malangizo ndi kuwala,+Komanso kudzudzula kumene kumathandiza munthu kusintha ndi njira yakumoyo.+
4 Inu anthu anga, ndimvereni.Iwe mtundu wanga,+ tchera khutu kwa ine. Chifukwa kwa ine kudzachokera lamulo+Ndipo ndidzachititsa kuti chilungamo changa chikhazikike ngati kuwala ku mitundu ya anthu.+
4 Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.+ Malembawa amatithandiza kupirira+ ndiponso amatilimbikitsa nʼcholinga choti tikhale ndi chiyembekezo.+
16 Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi othandiza pophunzitsa,+ kudzudzula, kukonza zinthu ndi kulangiza mwachilungamo,+ 17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera kwambiri ndi wokonzeka mokwanira kugwira ntchito iliyonse yabwino.
19 Nʼchifukwa chake sitikayikira ngakhale pangʼono kuti mawu aulosiwa adzakwaniritsidwa ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewa aziwala mʼmitima yanu ngati nyale+ imene ikuwala mumdima. Pitirizani kuchita zimenezi mpaka mʼbandakucha, nthanda*+ itatuluka.