-
Salimo 18:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Munthu wokhulupirika, mumamuchitira zinthu mokhulupirika.+
Munthu wopanda cholakwa, mumamuchitira zinthu mwachilungamo.+
-
Chivumbulutso 15:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Iwo ankaimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu ndi nyimbo ya Mwanawankhosa+ yakuti:
“Ntchito zanu nʼzazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova* Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama komanso zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+ 4 Popeza inu nokha Yehova* ndinu wokhulupirika, ndi ndani amene sadzakuopani komanso kulemekeza dzina lanu?+ Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzalambira pamaso panu,+ chifukwa iwo adziwa malamulo anu olungama.”
-
-
-