-
Deuteronomo 6:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 “Tsopano amenewa ndi malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wanu wandipatsa kuti ndikuphunzitseni, kuti muzikazitsatira mukawoloka mtsinje wa Yorodano nʼkupita mʼdziko limene mukukalitenga kuti likhale lanu, 2 kuti muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira malangizo ake komanso malamulo ake amene ndikukuuzani, inuyo, ana anu ndi zidzukulu zanu,+ masiku onse a moyo wanu, nʼcholinga choti mukhale ndi moyo nthawi yaitali.+
-
-
Deuteronomo 30:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Lero ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu. Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+ 20 Musankhe moyo pokonda Yehova Mulungu wanu,+ kumvera mawu ake ndi kukhala okhulupirika kwa iye,+ chifukwa iye ndi amene amapereka moyo ndipo angakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo kwa nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzalipereka kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.”+
-
-
1 Petulo 3:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Munthu “amene amakonda moyo wake komanso amafuna kumakhala moyo wabwino, ayenera kusamala kuti asamalankhule zoipa ndi lilime lake+ ndiponso kuti asamalankhule zachinyengo ndi milomo yake. 11 Ayenera kusiya kuchita zoipa+ nʼkumachita zabwino.+ Ayeneranso kuyesetsa kumakhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+ 12 Maso a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva mapemphero awo opembedzera,+ koma Yehova* amakwiyira anthu amene amachita zoipa.”+
-