Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 2:22-25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Pa nthawiyi Eli anali atakalamba kwambiri koma anamva zonse zimene ana ake ankachitira+ Aisiraeli onse. Anamvanso kuti ankagona ndi akazi amene ankatumikira pakhomo la chihema chokumanako.+ 23 Ndipo iye ankawauza kuti: “Mukuchitiranji zimenezi? Chifukwatu zimene anthu onse akundiuza zokhudza inu ndi zoipa zokhazokha. 24 Musatero ana anga, chifukwa nkhani zimene ndikumva, zimene anthu a Yehova akunena, si zabwino. 25 Munthu akachimwira mnzake, munthu wina akhoza kumuchonderera kwa Yehova,* koma akachimwira Yehova,+ angamupempherere ndi ndani?” Koma anawo sankamvera bambo awo ndipo tsopano Yehova anali atatsimikiza mtima kuti awaphe.+

  • 1 Samueli 8:1-3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Samueli atakalamba, anaika ana ake aamuna kuti akhale oweruza mu Isiraeli. 2 Mwana wake woyamba anali Yoweli, ndipo wachiwiri anali Abiya.+ Iwo anali oweruza ku Beere-seba. 3 Ana akewa sanatsatire chitsanzo chake. Iwo ankakonda kupeza phindu mwachinyengo,+ kulandira ziphuphu+ ndiponso kupotoza chilungamo.+

  • 2 Samueli 15:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Nthawi yomweyo, Davide anauza atumiki ake onse amene anali naye ku Yerusalemu kuti: “Konzekani msangamsanga! Tiyeni tithawe,+ chifukwa palibe amene angapulumuke mʼmanja mwa Abisalomu. Fulumirani! Chifukwa akhoza kutipeza nʼkutigonjetsa kenako nʼkupha anthu onse amumzindawu ndi lupanga!”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena