-
1 Samueli 15:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Samueli anati: “Kodi Yehova amasangalala ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina+ kuposa kumvera mawu a Yehova? Dikira ndikuuze! Kumvera kumaposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kumaposa mafuta+ a nkhosa zamphongo. 23 Chifukwa kupanduka+ nʼchimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza nʼchimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso kulambira mafano.* Popeza wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti ukhale mfumu.”+
-
-
Mika 6:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kodi Yehova adzasangalala ndi masauzande a nkhosa zamphongo?
Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande ambirimbiri?+
Kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba chifukwa cha zolakwa zanga,
Ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?+
8 Iye anakuuza munthu iwe zimene zili zabwino.
Kodi Yehova akufuna kuti uzichita* chiyani?
-