-
Mlaliki 9:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndaonanso chinthu china padziko lapansi pano kuti si nthawi zonse pamene anthu othamanga kwambiri amapambana pampikisano komanso pamene amphamvu amapambana pankhondo.+ Si nthawi zonse pamene anthu ochenjera amapeza chakudya, ndiponso si nthawi zonse pamene anthu anzeru amakhala ndi chuma.+ Komanso anthu odziwa zinthu, si nthawi zonse pamene zinthu zimawayendera bwino,+ chifukwa nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.
-
-
Yakobo 4:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Tamverani inu amene mumanena kuti: “Lero kapena mawa tipita kumzinda wakutiwakuti ndipo tikatha chaka kumeneko. Tikachita malonda kumeneko nʼkupeza phindu.”+ 14 Mumanena zimenezi chonsecho simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.+ Chifukwa muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa kenako nʼkuzimiririka.+
-