Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 12:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Koma muzidzadya zinthu zimenezi pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ Muzidzadya zinthuzi inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi ndi Mlevi amene akukhala mumzinda wanu.* Ndipo muzidzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi zochita zanu zonse.

  • Mlaliki 3:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndinaona kuti palibe chabwino kuposa kuti munthu asangalale ndi ntchito yake+ chifukwa imeneyo ndi mphoto yake.* Nanga ndi ndani amene angamuchititse kuti aone zimene zidzachitike iye atafa.+

  • Mlaliki 8:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Choncho ndinauza anthu kuti ndi bwino kusangalala+ chifukwa palibe chabwino kwa munthu padziko lapansi pano kuposa kudya, kumwa ndi kusangalala. Azichita zimenezi pamene akugwira ntchito mwakhama masiku onse a moyo wake,+ amene Mulungu woona wamupatsa padziko lapansi pano.

  • Machitidwe 14:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni+ wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri.+ Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena