-
1 Mafumu 18:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Kenako muitane dzina la mulungu wanu.+ Inenso ndiitana dzina la Yehova, ndipo Mulungu amene ayankhe potumiza moto asonyeza kuti ndi Mulungu woona.”+ Anthu onsewo atamva zimenezi anayankha kuti: “Zili bwino.”
25 Eliya anauza aneneri a Baala kuti: “Yambani ndinu kusankha ngʼombe imodzi nʼkuikonza chifukwa mulipo ambiri. Kenako muitane dzina la mulungu wanu koma musayatse moto.”
-