35 Chipululu ndi dziko louma zidzasangalala,+
Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa ambiri.+
2 Deralo lidzachitadi maluwa.+
Lidzasangalala ndipo lidzafuula chifukwa cha chisangalalo.
Lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni,+
Kukongola kwa Karimeli+ ndiponso kwa Sharoni.+
Anthu adzaona ulemerero wa Yehova ndi kukongola kwa Mulungu wathu.