Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 19:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Pa tsiku limenelo, padzakhala msewu waukulu+ wochokera ku Iguputo kupita ku Asuri. Anthu a ku Asuri adzapita ku Iguputo ndipo anthu a ku Iguputo adzapita ku Asuri. Aiguputo adzatumikira Mulungu limodzi ndi Asuri.

  • Yesaya 27:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pa tsiku limenelo nyanga yaikulu ya nkhosa idzalizidwa,+ ndipo anthu amene anali atatsala pangʼono kufa mʼdziko la Asuri+ ndi amene anamwazikana mʼdziko la Iguputo,+ adzabwera kudzagwadira Yehova mʼphiri loyera ku Yerusalemu.+

  • Yesaya 35:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+

      Inde msewu umene udzatchedwe Msewu Wopatulika.

      Munthu wodetsedwa sadzayenda mumsewu umenewo.+

      Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera.

      Palibe munthu wopusa amene adzayende mumsewu umenewo.

  • Yesaya 40:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Winawake akufuula mʼchipululu kuti:

      “Konzani njira ya Yehova!+

      Mulungu wathu mukonzereni msewu wowongoka+ wodutsa mʼchipululu.+

  • Yesaya 57:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndiyeno wina adzanena kuti, ‘Konzani msewu! Konzani msewu! Konzani njira!+

      Chotsani chopinga chilichonse panjira ya anthu anga.’”

  • Yeremiya 31:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Udziikire zizindikiro zamumsewu,

      Ndipo udziikire zikwangwani.+

      Maganizo ako akhale panjirayo, njira imene ukuyenera kuyendamo.+

      Bwerera iwe namwali wa Isiraeli. Bwerera kumizinda yakoyi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena