-
Maliko 1:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la mneneri Yesaya kuti: “(Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole* kukakukonzera njira.)*+ 3 Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.’”+ 4 Yohane Mʼbatizi anali mʼchipululu ndipo ankalalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+
-
-
Luka 3:3-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Choncho iye anapita mʼmidzi yonse yapafupi ndi Yorodano ndipo ankalalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ 4 Ankachita zimenezi mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la mawu a Mneneri Yesaya kuti: “Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.+ 5 Chigwa chilichonse chikwiriridwe, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zisalazidwe. Njira zokhotakhota zikhale zowongoka ndipo malo okumbikakumbika akhale osalaza bwino. 6 Anthu onse adzaona njira ya Mulungu yopulumutsira anthu.’”+
-