Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 60:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mʼdziko lako simudzamvekanso zachiwawa

      Mʼdziko lako simudzakhalanso kusakaza kapena kuwononga.+

      Mipanda yako udzaitcha Chipulumutso+ ndipo mageti ako udzawatcha Tamanda.

  • Yesaya 65:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Sadzamanga nyumba kuti wina azikhalamo,

      Kapena kudzala kuti ena adye.

      Chifukwa masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo,+

      Ndipo anthu anga osankhidwa adzasangalala mokwanira ndi ntchito ya manja awo.

  • Yeremiya 23:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Mʼmasiku a mfumu imeneyi, Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Isiraeli adzakhala motetezeka.+ Dzina la mfumuyi lidzakhala: Yehova Ndi Chilungamo Chathu.”+

  • Ezekieli 34:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ine ndidzachita pangano lamtendere ndi nkhosazo.+ Ndipo ndidzachotsa zilombo zolusa mʼdzikomo+ nʼcholinga choti nkhosazo zizidzakhala mʼchipululu zili zotetezeka ndipo zizidzagona munkhalango.+

  • Hoseya 2:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zilombo zakutchire mʼmalo mwa anthu anga,+

      Komanso ndi mbalame zouluka mumlengalenga ndi zinthu zokwawa panthaka.+

      Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo mʼdzikolo.+

      Ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena