Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 10:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ana a Semu anali Elamu,+ Ashuri,+ Aripakisadi,+ Ludi ndi Aramu.+

  • Yesaya 21:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Ndauzidwa masomphenya ochititsa mantha akuti:

      Mtundu wachinyengo ukuchita zachinyengo,

      Ndipo mtundu wowononga ukuwononga.

      Pita ukachite nkhondo, iwe Elamu! Kazungulire mzindawo, iwe Mediya!+

      Ndidzathetsa mavuto onse amene mzindawo unachititsa.+

  • Yeremiya 25:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho ndinatenga kapu imene inali mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako. Mitunduyo ndi iyi:+

  • Yeremiya 25:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 mafumu onse a Zimiri, mafumu onse a Elamu,+ mafumu onse a Amedi,+

  • Ezekieli 32:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Elamu+ ali kumandako limodzi ndi gulu la anthu ake onse amene ankamutsatira ndipo anthuwo azungulira manda ake. Onsewo anaphedwa ndi lupanga. Iwo anatsikira kunthaka ali osadulidwa. Anthu amenewa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha. Tsopano anthu amenewa adzachita manyazi limodzi ndi anthu amene akutsikira kudzenje.*

  • Danieli 8:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndikuona masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili kunyumba yachifumu* ku Susani,+ imene ili mʼchigawo cha Elamu.+ Ndinaona masomphenyawa kuti ndinali mʼmphepete mwa mtsinje wa Ulai.

  • Machitidwe 2:8, 9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndiye zikutheka bwanji kuti aliyense pagulu lathuli akumva chilankhulo chake? 9 Pano pali Apati, Amedi+ ndi Aelamu.+ Palinso anthu ochokera ku Mesopotamiya, ku Yudeya, ku Kapadokiya, ku Ponto ndi kuchigawo cha Asia.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena