Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 9:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Nyumbayi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi adzayangʼana modabwa ndipo adzaimba mluzu nʼkunena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova anachitira zimenezi dzikoli komanso nyumbayi?’+

  • 2 Mbiri 36:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ mʼnyumba yopatulika.+ Sinamvere chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena wodwala.+ Mulungu anapereka zonse mʼmanja mwake.+

  • 2 Mbiri 36:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Inatentha nyumba ya Mulungu woona,+ kugwetsa mpanda wa Yerusalemu,+ kutentha nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso zinthu zonse zamtengo wapatali.+

  • Salimo 74:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Iwo limodzi ndi ana awo ananena mumtima mwawo kuti:

      “Malo onse amene anthu amalambirirako Mulungu mʼdzikoli, ayenera kutenthedwa.”

  • Salimo 79:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa mʼdziko limene ndi cholowa chanu.+

      Aipitsa kachisi wanu woyera.+

      Yerusalemu amusandutsa bwinja.+

  • Yeremiya 26:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mika+ wa ku Moreseti nayenso ankanenera mʼmasiku a Mfumu Hezekiya+ ya ku Yuda. Iye ankauza anthu onse a ku Yuda kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:

      “Ziyoni adzalimidwa ngati munda,

      Yerusalemu adzakhala mabwinja,+

      Ndipo phiri la nyumba ya Mulungu* lidzakhala ngati zitunda zamunkhalango.”’+

  • Maliro 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Yehova wakana guwa lake lansembe.

      Iye wasiya malo ake opatulika.+

      Wapereka mʼmanja mwa adani makoma a nsanja zake zotetezeka.+

      Adaniwo afuula mʼnyumba ya Yehova+ ngati pa tsiku lachikondwerero.

  • Ezekieli 24:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 ‘Uza nyumba ya Isiraeli kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatsala pangʼono kudetsa malo anga opatulika,+ chinthu chimene mumachinyadira kwambiri, chinthu chimene mumachikonda komanso chapamtima panu. Ana anu aamuna ndi aakazi amene munawasiya mumzindawo adzaphedwa ndi lupanga.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena