-
Deuteronomo 30:1-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 “Mawu onsewa akadzakwaniritsidwa pa inu, madalitso ndi matemberero amene ndaika pamaso panu,+ ndipo mukadzawakumbukira*+ muli ku mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsireni,+ 2 inu nʼkubwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ komanso kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu,+ 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+ 4 Ngakhale anthu a mtundu wanu amene anabalalitsidwawo atadzakhala kumalekezero kwa thambo, Yehova Mulungu wanu adzakusonkhanitsani nʼkukubweretsani kuchokera kumeneko.+
-
-
1 Mafumu 8:47, 48Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 ndiyeno iwo nʼkuzindikira kulakwa kwawo mʼdziko limene anawatengeralo+ nʼkulapa,+ ndiponso akapempha chifundo kwa inu mʼdziko la adani awowo+ nʼkunena kuti, ‘Tachimwa, talakwitsa ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 48 nʼkubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse,+ mʼdziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayangʼana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, mzinda umene mwasankha komanso nyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+
-