Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ine ndidzalola kuti Farao aumitse mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzalemekeza dzina langa pogonjetsa Farao ndi gulu lake lonse lankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi zomwezo.

  • 2 Mafumu 19:17-19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Nʼzoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko ndi anthu a mʼmayikowo.+ 18 Aponya milungu yawo pamoto, chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala. Nʼchifukwa chake anatha kuiwononga. 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, chonde tipulumutseni mʼmanja mwake, kuti maufumu onse apadziko lapansi adziwe kuti inu nokha Yehova, ndinu Mulungu.”+

  • Salimo 83:17, 18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Achititsidwe manyazi ndipo akhale ndi mantha mpaka kalekale.

      Anyozeke ndipo atheretu.

      18 Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+

      Inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.+

  • Ezekieli 39:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 ‘Ndidzasonyeza ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina ndipo mitundu yonse ya anthu idzaona chiweruzo chimene ndapereka komanso mphamvu zimene* ndasonyeza pakati pawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena