2 Ndine wosangalala kukuuzani zizindikiro ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wamʼmwambamwamba wandichitira. 3 Zizindikiro zake nʼzazikulu ndipo zochita zake nʼzamphamvu. Ufumu wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ulamuliro wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+