28 Mfumuyo itakambirana ndi anthu ena inapanga ana awiri a ngʼombe agolide,+ kenako inauza anthu onse kuti: “Ndikuona kuti mukuvutika kwambiri kupita ku Yerusalemu. Ndiye ndakupangirani Mulungu uyu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo+ Aisiraeli inu.”