Yeremiya 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pita, ndipo ukalengeze mawu awa kumpoto:+ ‘Yehova wanena kuti:+ “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya+ chifukwa ndine wokhulupirika,” akutero Yehova. “Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. Zekariya 1:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Uwauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Bwererani kwa ine,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, “ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’” Yakobo 4:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.+ Yeretsani manja anu ochimwa inu,+ ndipo yeretsani mitima yanu+ okayikakayika inu.
12 Pita, ndipo ukalengeze mawu awa kumpoto:+ ‘Yehova wanena kuti:+ “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya+ chifukwa ndine wokhulupirika,” akutero Yehova. “Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.
3 Uwauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Bwererani kwa ine,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, “ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’”
8 Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.+ Yeretsani manja anu ochimwa inu,+ ndipo yeretsani mitima yanu+ okayikakayika inu.