Levitiko 19:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Uza gulu lonse la Aisiraeli kuti, ‘Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.+ Deuteronomo 18:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Mukhale opanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+ Luka 6:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 Pitirizani kukhala achifundo, mofanana ndi Atate wanu amenenso ndi wachifundo.+ 1 Petulo 1:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+