Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 12:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Pa tsiku loyamba muzidzachita msonkhano wopatulika, ndipo pa tsiku la 7 muzidzachitanso msonkhano wina wopatulika. Masiku amenewa musamadzagwire ntchito.+ Koma chakudya choti munthu aliyense adye, chimenecho chokha muzidzaphika.

  • Deuteronomo 23:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mnzanu, mungathe kupulula ndi dzanja lanu tirigu amene wacha, koma musamamwete ndi chikwakwa tirigu wa mnzanu.”+

  • Maliko 2:23-28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Yesu akudutsa mʼminda ya tirigu pa tsiku la Sabata, ophunzira ake anayamba kubudula ngala za tirigu nʼkumadya.+ 24 Choncho Afarisi anamuuza kuti: “Taona! Nʼchifukwa chiyani akuchita zinthu zimene ndi zosayenera kuchita pa Sabata?” 25 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala ndipo analibiretu chilichonse?+ 26 Nkhani yonena za Abiyatara+ wansembe wamkulu imanena kuti, Davide analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* umene aliyense sankayenera kudya malinga ndi malamulo koma ansembe okha.+ Iye anatenga mitanda ina ya mkatewo nʼkupatsa amuna amene anali naye limodzi. Kodi inu simunawerenge nkhani imeneyi?” 27 Kenako anawauza kuti: “Sabata linakhalako chifukwa cha munthu,+ osati munthu chifukwa cha Sabata. 28 Choncho Mwana wa munthu ndi Mbuye wa Sabata.”+

  • Luka 6:1-5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tsiku lina pa tsiku la sabata, Yesu ankadutsa mʼmunda wa tirigu ndipo ophunzira ake ankabudula ngala za tirigu+ nʼkumazitikita mʼmanja mwawo kenako nʼkudya.+ 2 Afarisi ena ataona zimenezi anati: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zimene ndi zosayenera kuchita pa Sabata?”+ 3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala?+ 4 Kodi simunawerenge kuti analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* imene iye ndi anthu omwe anali nawo aja sankayenera kudya malinga ndi malamulo, koma ansembe okha?”+ 5 Kenako anapitiriza kuwauza kuti: “Mwana wa munthu ndi Mbuye wa Sabata.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena