-
Maliko 14:37-42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Atatero anabwerera ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Simoni, zoona ukugona? Kodi unalibe mphamvu kuti ukanakhalabe maso kwa ola limodzi?+ 38 Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 39 Atatero anachokanso kupita kukapemphera ndipo ananenanso mawu omwe aja.+ 40 Anabweranso nʼkuwapeza akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera, choncho iwo anasowa chomuyankha. 41 Anabweranso kachitatu nʼkuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula? Basi! Nthawi yakwana!+ Taonani! Mwana wa munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. 42 Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+
-