-
Mateyu 13:54-58Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
54 Atafika mʼdera lakwawo+ anayamba kuwaphunzitsa musunagoge wawo, moti anthu anadabwa ndipo ananena kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru ndi ntchito zamphamvu zoterezi anazitenga kuti?+ 55 Kodi uyu si mwana wa kalipentala uja?+ Kodi mayi ake si Mariya, ndipo azichimwene ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi?+ 56 Ndipo azichemwali ake onse sitili nawo konkuno? Nanga iyeyu zinthu zonsezi anazitenga kuti?”+ 57 Choncho anayamba kukhumudwa naye.+ Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo kapena mʼnyumba mwake, koma kwina.”+ 58 Ndipo sanachite ntchito zamphamvu zambiri kumeneko chifukwa chakuti anthuwo analibe chikhulupiriro.
-