-
Mateyu 22:23-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Pa tsiku limenelo Asaduki amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 24 “Mphunzitsi, Mose ananena kuti: ‘Ngati mwamuna wamwalira asanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+ 25 Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako nʼkumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkaziyo anakwatiwa ndi mchimwene wa mwamuna wake uja. 26 Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja. 27 Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 28 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.”
-
-
Luka 20:27-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Koma Asaduki ena, amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 28 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti, ‘Ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma sanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+ 29 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira asanabereke mwana. 30 Wachiwirinso chimodzimodzi. 31 Kenako wachitatu anamukwatira. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja, onse anamwalira osasiya ana. 32 Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 33 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.”
-