21 Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa.+ Ndiye pamene ankapemphera, kumwamba kunatseguka,+ 22 ndipo mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unatsika kudzamutera. Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.”+