-
Yohane 1:32-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba ndipo unakhalabe pa iye.+ 33 Inenso sindinkamudziwa, koma Mulungu amene anandituma kudzabatiza mʼmadzi anandiuza kuti: ‘Ukadzaona mzimu ukutsika nʼkukhazikika pamunthu wina,+ ameneyo ndi amene amabatiza ndi mzimu woyera.’+ 34 Ine ndinaonadi zimenezo ndipo ndachitira umboni kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+
-