-
Mateyu 10:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Mayina a atumwi 12 ndi awa:+ Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo*+ ndi Andireya+ mchimwene wake. Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+ 3 Filipo ndi Batolomeyo,+ Tomasi+ ndi Mateyu+ wokhometsa msonkho, Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Tadeyo. 4 Simoni Kananiya* ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anapereka Yesu.+
-
-
Maliko 3:14-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndiyeno anasankha gulu la anthu 12, amenenso anawapatsa dzina lakuti atumwi, kuti aziyenda naye nthawi zonse komanso kuti aziwatuma kukalalikira 15 nʼkuwapatsa mphamvu zoti azitulutsa ziwanda.+
16 Mʼgulu la anthu 12+ amene anasankha aja munali Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo,+ 17 Yakobo mwana wa Zebedayo ndi Yohane mchimwene wake wa Yakobo (awiriwa anawapatsanso dzina lakuti Boanege, limene limatanthauza “Ana a Bingu”),+ 18 Andireya, Filipo, Batolomeyo, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19 ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anadzamʼpereka.
Kenako Yesu analowa mʼnyumba.
-