Salimo 107:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Chifukwa iye wathetsa ludzu la anthu aludzuNdipo anthu anjala wawadyetsa zinthu zabwino.+ Yesaya 55:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 55 Inu nonse amene mukumva ludzu,+ bwerani mudzamwe madzi.+ Inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule kuti mudye. Inde bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka+ popanda ndalama ndiponso popanda mtengo.+ Yeremiya 31:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Chifukwa ndidzapereka mphamvu kwa munthu wotopa ndipo ndidzalimbikitsa aliyense amene wafooka.”+ Mateyu 5:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Osangalala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu+ la chilungamo chifukwa adzakhuta.+
55 Inu nonse amene mukumva ludzu,+ bwerani mudzamwe madzi.+ Inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule kuti mudye. Inde bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka+ popanda ndalama ndiponso popanda mtengo.+