-
Mateyu 26:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Iye anati: “Pitani mumzinda kwa Munthu wakutiwakuti ndipo mukamuuze kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Nthawi yanga yoikidwiratu yayandikira. Ndidzachita phwando la Pasika pamodzi ndi ophunzira anga kunyumba kwako.”’” 19 Choncho ophunzirawo anachitadi mogwirizana ndi zimene Yesu anawauza ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.
-
-
Maliko 14:13-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno Yesu anatuma awiri mwa ophunzira akewo nʼkuwauza kuti: “Pitani mumzinda ndipo mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire,+ 14 ndipo mʼnyumba imene akalowe, mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 15 Iye akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukatikonzere Pasika mmenemo.” 16 Choncho ophunzirawo anapita nʼkulowa mumzinda ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo kumeneko anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.
-