-
Luka 22:10-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Iye anawayankha kuti: “Mukalowa mumzinda, mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire mʼnyumba imene akalowe.+ 11 Ndipo mukauze mwininyumba imeneyo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 12 Ndiyeno munthu ameneyo akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukakonzere mmenemo.” 13 Choncho ananyamuka ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.
-