-
Yesaya 53:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa,+
Mofanana ndi nkhosa yaikazi imene yangokhala chete pamene akufuna kuimeta ubweya,
Ndipo sanatsegule pakamwa pake.+
8 Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.
Ndi ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mʼbadwo wa makolo ake?*
Popeza iye anadulidwa mʼdziko la anthu amoyo.+
-