-
Machitidwe 26:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ndipo ndidzakupulumutsa kwa anthu awa komanso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutumiza+ 18 kuti ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mumdima+ nʼkuwapititsa kowala+ ndiponso kuwachotsa mʼmanja mwa Satana+ nʼkuwapititsa kwa Mulungu. Ukachite zimenezi kuti machimo awo akhululukidwe+ nʼkulandira cholowa pamodzi ndi oyeretsedwa chifukwa chondikhulupirira.’
-
-
2 Akorinto 4:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ngati uthenga wabwino umene tikulalikira uli wophimbika, ndi wophimbika kwa anthu amene akupita kukawonongedwa, 4 anthu osakhulupirira amene mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo awo+ kuti asaone kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero wonena za Khristu, yemwe ndi chifaniziro cha Mulungu.+
-
-
Aefeso 2:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Kuwonjezera pamenepo, Mulungu anapangitsa kuti mukhale amoyo ngakhale kuti munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu komanso machimo anu.+ 2 Pa nthawi ina munkachita zimenezi mogwirizana ndi nthawi* za mʼdzikoli,+ pomvera wolamulira wa mpweya+ umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe+ kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana osamvera.
-